10. Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?
11. Kulingalira kwa munthu kucedwetsa mkwiyo;Ulemerero wace uli wakuti akhululukire colakwa.
12. Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;Koma kukoma mtima kwace kunga mame pamsipu.
13. Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wace;Ndipo makangano a mkazi ndiwo kudontha-donthabe.
14. Nyumba ndi cuma ndizo colowa ca atate;Koma mkazi wanzeru acokera kwa Yehova.
15. Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;Ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.
16. Wosunga lamulo asunga moyo wace;Wonyalanyaza mayendedwe ace adzafa.
17. Wocitira waumphawi cifundo abwereka Yehova;Adzambwezera cokoma caceco.
18. Menya mwanako, ciyembekezero ciripo,Osafunitsa kumuononga.
19. Munthu waukali alipire mwini;Pakuti ukampulumutsa udzateronso.