Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 19:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?

11. Kulingalira kwa munthu kucedwetsa mkwiyo;Ulemerero wace uli wakuti akhululukire colakwa.

12. Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;Koma kukoma mtima kwace kunga mame pamsipu.

13. Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wace;Ndipo makangano a mkazi ndiwo kudontha-donthabe.

14. Nyumba ndi cuma ndizo colowa ca atate;Koma mkazi wanzeru acokera kwa Yehova.

15. Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;Ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.

16. Wosunga lamulo asunga moyo wace;Wonyalanyaza mayendedwe ace adzafa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 19