Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 19:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wosauka woyenda mwangwiroAposa wokhetsa milomo ndi wopusa.

2. Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino;Ndipo wofulumira ndi mapazi ace amacimwa.

3. Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yace;Mtima wace udandaula pa Yehova.

4. Cuma cionjezetsa mabwenzi ambiri;Koma mnzace wa waumphawi amleka.

5. Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;Wolankhula mabodza sadzapulumuka.

6. Ambiri adzapembedza waufulu;Ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.

7. Abale onse a wosauka amuda;Nanga mabwenzi ace kodi satanimphirana naye?Awatsata ndi mau, koma kuli zi.

8. Wolandira nzeru akonda moyo wace;Wosunga luntha adzapeza zabwino.

9. Mboni yonama sidzapulumuka cilango;Wolankhula mabodza adzaonongeka.

10. Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?

Werengani mutu wathunthu Miyambi 19