8. Wolandira cokometsera mlandu aciyesa ngale;Pali ponse popita iye acenjera.
9. Wobisa colakwa afunitsa cikondano;Koma wobwereza-bwereza mau afetsa ubwenzi.
10. Cidzudzulo cilowa m'kati mwa wozindikira,Kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.
11. Woipa amafuna kupanduka kokha;Koma adzamtumizira mthenga wankhanza.
12. Kukomana ndi citsiru m'kupusa kwaceKuopsya koposa cirombo cocicotsera anace.
13. Wobwezera zabwino zoipa,Zoipa sizidzamcokera kwao.