5. Wocitira ciphwete aumphawi atonza Mlengi;Wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka cilango.
6. Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;Ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.
7. Mlomo wangwiro suyenera citsiru;Ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.
8. Wolandira cokometsera mlandu aciyesa ngale;Pali ponse popita iye acenjera.
9. Wobisa colakwa afunitsa cikondano;Koma wobwereza-bwereza mau afetsa ubwenzi.
10. Cidzudzulo cilowa m'kati mwa wozindikira,Kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.
11. Woipa amafuna kupanduka kokha;Koma adzamtumizira mthenga wankhanza.
12. Kukomana ndi citsiru m'kupusa kwaceKuopsya koposa cirombo cocicotsera anace.
13. Wobwezera zabwino zoipa,Zoipa sizidzamcokera kwao.