Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 17:16-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la citsiru,Popeza wopusa alibe mtima?

17. Bwenzi limakonda nthawi zonse;Ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.

18. Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,Napereka cikole pamaso pa mnzace.

19. Wokonda ndeu akonda kulakwa;Ndipo wotarikitsa khomo lace afunafuna kuonongeka.

20. Wokhota mtima sadzapeza bwinoNdipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.

21. Wobala citsiru adzicititsa cisoni;Ndipo atate wa wopusa sakondwa.

22. Mtima wosekerera uciritsa bwinoKoma mzimu wosweka uphwetsa mafupa,

23. Munthu woipa alandira cokometsera mlandu coturutsa m'mfunga,Kuti apambukitse mayendedwe a ciweruzo.

24. Nzeru iri pamaso pa wozindikira;Koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.

25. Mwana wopusa acititsa atate wace cisoni,Namvetsa zowawa amace wombala.

26. Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino,Ngakhale kukwapula akuru cifukwa aongoka mtima.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 17