Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 17:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cidzudzulo cilowa m'kati mwa wozindikira,Kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.

11. Woipa amafuna kupanduka kokha;Koma adzamtumizira mthenga wankhanza.

12. Kukomana ndi citsiru m'kupusa kwaceKuopsya koposa cirombo cocicotsera anace.

13. Wobwezera zabwino zoipa,Zoipa sizidzamcokera kwao.

14. Ciyambi ca ndeu cifanana ndi kutsegulira madzi;Tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.

15. Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama,Onse awiriwa amnyansa Yehova.

16. Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la citsiru,Popeza wopusa alibe mtima?

17. Bwenzi limakonda nthawi zonse;Ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.

18. Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,Napereka cikole pamaso pa mnzace.

19. Wokonda ndeu akonda kulakwa;Ndipo wotarikitsa khomo lace afunafuna kuonongeka.

20. Wokhota mtima sadzapeza bwinoNdipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 17