Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 17:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nyenyeswa youma, pokhala mtendere,Iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano.

2. Kapolo wocitamwanzeruAdzalamulira mwana wocititsa manyazi,Nadzagawana nao abale colowa.

3. Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golidi ali ndi ng'anjo;Koma Yehova ayesa mitima.

4. Wocimwa amasamalira milomo yolakwa;Wonama amvera lilime losakaza.

5. Wocitira ciphwete aumphawi atonza Mlengi;Wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka cilango.

6. Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;Ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

7. Mlomo wangwiro suyenera citsiru;Ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.

8. Wolandira cokometsera mlandu aciyesa ngale;Pali ponse popita iye acenjera.

9. Wobisa colakwa afunitsa cikondano;Koma wobwereza-bwereza mau afetsa ubwenzi.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 17