5. Yense wonyada mtima anyansa Yehova;Zoonadi sadzapulumuka cilango.
6. Mphulupulu iomboledwa ndi cifundo ndi ntheradi;Apatuka pa zoipa poopa Yehova.
7. Njira za munthu zikakonda Yehova,Ayanjanitsana naye ngakhale adani ace.
8. Zapang'ono, pokhala cilungamo,Ziposa phindu lalikuru lopanda ciweruzo.
9. Mtima wa munthu ulingalira njira yace;Koma Yehova ayendetsa mapazi ace.
10. Mau a mlauli ali m'milomo ya mfumu;M'kamwa mwace simudzacita cetera poweruza.
11. Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova;Ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m'thumba.
12. Kucita mphulupulu kunyansa mafumu;Pakuti mpando wao wakhazikika ndi cilungamo.
13. Milomo yolungama ikondweretsa mafumu;Wonena zoongoka amkonda.
14. Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa;Wanzeru adzaukhulula.
15. M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo;Kukoma mtima kwace kunga mtambo wa mvula ya masika.
16. Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golidi,Kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
17. Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;Wosunga njira yace acinjiriza moyo wace.