Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 16:24-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Mau okoma ndiwo cisa ca uci,Otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.

25. Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka,Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.

26. Wanchito adzigwirira yekha nchito;Pakuti m'kamwa mwace mumfulumiza.

27. Munthu wopanda pace akonzeratu zoipa;Ndipo m'milomo mwace muli moto wopsereza.

28. Munthu wokhota amautsa makani;Kazitape afetsa ubwenzi.

29. Munthu waciwawa akopa mnzace,Namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.

30. Wotsinzina ndiye aganizira zakhota;Wosunama afikitsa zoipa.

31. Imvi ndiyo korona wa ulemu,Idzapezedwa m'njira ya cilungamo.

32. Wosakwiya msanga aposa wamphamvu;Wolamulira mtima wace naposa wolanda mudzi.

33. Maere aponyedwa pamfunga;Koma ndiye Yehova alongosola zonse.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 16