Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 16:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Kunyada kutsogolera kuonongekaMtinia wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.

19. Kufatsa mtima ndi osaukaKuposa kugawana zofunkha ndi onyada.

20. Wolabadira mau adzapeza bwino;Ndipo wokhulupirira Yehova adala.

21. Wanzeru mtima adzachedwa wocenjera;Ndipo kukoma kwa milomo kuyenjezera kuphunzira.

22. Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wace;Koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.

23. Mtima wa wanzeru ucenjeza m'kamwa mwace,Nuphunzitsanso milomo yace.

24. Mau okoma ndiwo cisa ca uci,Otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.

25. Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka,Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.

26. Wanchito adzigwirira yekha nchito;Pakuti m'kamwa mwace mumfulumiza.

27. Munthu wopanda pace akonzeratu zoipa;Ndipo m'milomo mwace muli moto wopsereza.

28. Munthu wokhota amautsa makani;Kazitape afetsa ubwenzi.

29. Munthu waciwawa akopa mnzace,Namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 16