23. Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa;Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.
24. Comwe woipa aciopa cidzamfikira;Koma comwe olungama acifuna cidzapatsidwa.
25. Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi;Koma olungama ndiwo maziko osatha.
26. Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.
27. Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;Koma zaka za oipa zidzafinimpha,
28. Ciyembekezo ca olungama ndico cimwemwe;Koma cidikiro ca oipa cidzaonongeka.
29. Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;Koma akucita zoipa adzaonongeka.