Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 10:2-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Cuma ca ucimo sicithangata:Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.

3. Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama;Koma amainga cifuniro ca wocimwa.

4. Wocita ndi dzanja laulesi amasauka;Koma dzanja la akhama lilemeretsa.

5. Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru;Koma wogona pakututa ndi mwana wocititsa manyazi.

6. Madalitso ali pamtu pa wolungamaKoma m'kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.

7. Amayesa wolungama wodala pamkumbukira;Koma dzina la oipa lidzabvunda.

8. Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo;Koma citsiru colongolola cidzagwa.

9. Woyenda moongoka amayenda osatekeseka;Koma wokhotetsa njira zace adzadziwika.

10. Wotsinzinira acititsa cisoni;Koma wodzudzula momveka acita mtendere.

11. M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo;Koma m'kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.

12. Udani upikisanitsa;Koma cikondi cikwirira zolakwa zonse.

13. Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira;Koma wopusa pamsana pace ntyole.

14. Anzeru akundika zomwe adziwaKoma m'kamwa mwa citsiru muononga tsopano lino.

15. Cuma ca wolemera ndi mudzi wace wolimba;Koma umphawi wao uononga osauka.

16. Nchito za wolungama zipatsa moyo;Koma phindu la oipa licimwitsa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 10