Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 10:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Wobisa udani ali ndi milomo yonama;Wonena ugogodi ndiye citsiru.

19. Pocuruka mau zolakwa sizisoweka;Koma wokhala cete acita mwanzeru.

20. Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;Koma mtima wa oipa uli wacabe.

21. Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;Koma zitsiru zimafa posowa nzeru.

22. Madalitso a Yehova alemeretsa,Saonjezerapo cisoni.

23. Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa;Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.

24. Comwe woipa aciopa cidzamfikira;Koma comwe olungama acifuna cidzapatsidwa.

25. Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi;Koma olungama ndiwo maziko osatha.

26. Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.

27. Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;Koma zaka za oipa zidzafinimpha,

28. Ciyembekezo ca olungama ndico cimwemwe;Koma cidikiro ca oipa cidzaonongeka.

29. Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;Koma akucita zoipa adzaonongeka.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 10