Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 10:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Cuma ca wolemera ndi mudzi wace wolimba;Koma umphawi wao uononga osauka.

16. Nchito za wolungama zipatsa moyo;Koma phindu la oipa licimwitsa.

17. Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo;Koma wosiya cidzudzulo asocera.

18. Wobisa udani ali ndi milomo yonama;Wonena ugogodi ndiye citsiru.

19. Pocuruka mau zolakwa sizisoweka;Koma wokhala cete acita mwanzeru.

20. Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;Koma mtima wa oipa uli wacabe.

21. Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;Koma zitsiru zimafa posowa nzeru.

22. Madalitso a Yehova alemeretsa,Saonjezerapo cisoni.

23. Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa;Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.

24. Comwe woipa aciopa cidzamfikira;Koma comwe olungama acifuna cidzapatsidwa.

25. Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi;Koma olungama ndiwo maziko osatha.

26. Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.

27. Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;Koma zaka za oipa zidzafinimpha,

Werengani mutu wathunthu Miyambi 10