Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 6:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mau a Yehova aitana mudzi, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.

10. Kodi m'nyumba ya woipa mukali cuma cosalungama, ndi muyeso wocepa umene ayenera kuipidwa nao?

11. Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?

12. Pakuti anthu ace olemera adzala ndi ciwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limacita monyenga m'kamwa mwao.

13. Cifukwa cace Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula cifukwa ca zocimwa zako.

14. Udzadya koma osakhuta; ndi njala yako idzakhala pakati pako; ndipo udzacotsa koma osalanditsa; ndi ici wacilanditsa ndidzacipereka kulupanga.

Werengani mutu wathunthu Mika 6