Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 6:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba cifukwa ca kulakwa kwanga, cipatso ca thupi langa cifukwa ca kucimwa kwa moyo wanga?

8. Iye anakuuza, munthuwe, comwe ciri cokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti ucite colungama, ndi kukonda cifundo ndi kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako?

9. Mau a Yehova aitana mudzi, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.

10. Kodi m'nyumba ya woipa mukali cuma cosalungama, ndi muyeso wocepa umene ayenera kuipidwa nao?

11. Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?

Werengani mutu wathunthu Mika 6