Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 6:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Kodi m'nyumba ya woipa mukali cuma cosalungama, ndi muyeso wocepa umene ayenera kuipidwa nao?

11. Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?

12. Pakuti anthu ace olemera adzala ndi ciwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limacita monyenga m'kamwa mwao.

13. Cifukwa cace Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula cifukwa ca zocimwa zako.

14. Udzadya koma osakhuta; ndi njala yako idzakhala pakati pako; ndipo udzacotsa koma osalanditsa; ndi ici wacilanditsa ndidzacipereka kulupanga.

15. Udzafesa koma osaceka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.

16. Pakuti asunga malemba a Omri, ndi nchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda m'uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo cotsonya; ndipo mudzasenza citonzo ca anthu anga.

Werengani mutu wathunthu Mika 6