Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 99:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.

2. Yehova ndiye wamkuru m'Ziyoni;Ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

3. Alemekeze dzina lanu lalikuru ndi loopsa;Ili ndilo loyera.

4. Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda ciweruzo;Inu mukhazikitsa zolunjika,Mucita ciweruzo ndi cilungamo m'Yakobo.

5. Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,Ndipo padirani poponderapo mapasa ace:Iye ndiye Woyera.

6. Mwa ansembe ace muli Mose ndi Aroni,Ndi Samueli mwa iwo akuitanira dzina lace;Anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 99