Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 97:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova acita ufumu; dziko lapansi likondwere;Zisumbu zambiri zikondwerere.

2. Pomzinga pali mitambo ndi mdima;Cilungamo ndi ciweruzo ndizo zolimbitsa mpando wacifumu wace.

3. Moto umtsogolera,Nupsereza otsutsana naye pozungulirapo,

4. Mphezi zace zinaunikira dziko lokhalamo anthu;Dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.

5. Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

6. Kumwamba kulalikira cilungamo cace,Ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wace.

7. Onse akutumikira fano losema,Akudzitamandira nao mafano, acite manyazi:Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

8. Ziyoni anamva nakondwera,Nasekerera ana akazi a Yuda;Cifukwa ca maweruzo anu, Yehova.

9. Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,Ndinu wokwezeka kwakukuru pamwamba pa milungu yonse yina.

10. Inuokonda Yehova, danani naco coipa:Iye asunga moyo wa okondedwa ace;Awalanditsa m'manja mwa oipa.

11. Kuunika kufesekera wolungama, Ndi cikondwerero oongoka mtima.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 97