Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 95:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Nyanja ndi yace, anailenga;Ndipo manja ace anaumba dziko louma.

6. Tiyeni, tipembedze tiwerame;Tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga:

7. Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu,Ndipo ife ndife anthu a pabusa pace, ndi nkhosa za m'dzanja mwace.Lero, mukamva mau acel

8. Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba,Ngati tsiku la ku Masa m'cipululu;

9. Pamene makolo anu anandisuntha,Anandiyesa, anapenyanso cocita Ine.

10. Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa cisoni,Ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima,Ndipo sadziwa njira zanga.

11. Cifukwa cace ndinalumbira mu mkwiyo wanga,Ngati adzalowa mpumulo wanga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 95