Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 95:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tiyeni tiyimbire Yehova mokondwera;Tipfuule kwa thanthwe la cipulumutso cathu.

2. Tidze naco ciyamiko pamaso pace,Timpfuulire Iye mokondwera ndi masalmo.

3. Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkuru;Ndi mfumu yaikuru yoposa milungu yonse.

4. Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lace;Cuma ca m'mapiri comwe ndi cace.

5. Nyanja ndi yace, anailenga;Ndipo manja ace anaumba dziko louma.

6. Tiyeni, tipembedze tiwerame;Tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga:

7. Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu,Ndipo ife ndife anthu a pabusa pace, ndi nkhosa za m'dzanja mwace.Lero, mukamva mau acel

Werengani mutu wathunthu Masalmo 95