Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 93:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova acita ufumu; wadzibveka ndi ukulu;Wadzibveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'cuuno;Dziko lomwe lokhalamo anthu likhazikika, silidzagwedezeka.

2. Mpando wacifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija;Inu ndinu wosayambira ndi kale, lomwe.

3. Mitsinje ikweza, Yehova,Mitsinje ikweza mkokomo wao;Mitsinje ikweza mafunde ao.

4. Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu,Wakuposa mkokomo wa madzi ambiri,Ndi mafunde olimba a nyanja.

5. Mboni zanu zibvomerezeka ndithu;Ciyero ciyenera nyumba yanu, Yehova, ku nthawi za muyaya.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 93