Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 89:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova?Ndipo cikhulupiriko canu cikuzingani.

9. Inu ndinu wakucita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja;Pakuuka mafunde ace muwacititsa bata.

10. Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa;Munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.

11. Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu;Munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwace.

12. Munalenga kumpoto ndi kumwela;Tabora ndi Hermoni apfuula mokondwera m'dzina lanu.

13. Muli nao mkono wanu wolimba;M'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.

14. Cilungamo ndi ciweruzo ndiwo maziko a mpando wacifumu wanu;Cifundo ndi coonadi zitsogolera pankhope panu.

15. Odala anthu odziwa liu la lipenga;Ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

16. Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse;Ndipo akwezeka m'cilungamo canu.

17. Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;Ndipo potibvomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 89