Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 89:39-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Munakaniza cipangano ca mtumiki wanu;Munaipsa korona wace ndi kumponya pansi,

40. Munapasula maguta ace onse;Munagumula malinga ace.

41. Onse opita panjirapa amfunkhira:Akhala cotonza ca anansi ace.

42. Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;Munakondweretsa adani ace onse.

43. Munapinditsa kukamwa kwace kwa lupanga lace,Osamuimika kunkhondo.

44. Munaleketsa kuwala kwace,Ndipo munagwetsa pansi mpando wacifumu wace.

45. Munafupikitsa masiku a mnyamata wace;Munamkuta nao manyazi.

46. Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova;Ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?

47. Kumbukilani kuti nthawi yanga njapafupi;Munalengeranji ana onse a anthu kwacabe?

48. Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa?Amene adzapulumutsa moyo wace ku mphamvu ya manda?

49. Ciri kuti cifundo canu cakale, Ambuye,Munacilumbirira Davide pa cikhulupiriko canu?

Werengani mutu wathunthu Masalmo 89