Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 89:28-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndidzamsungira cifundo canga ku nthawi yonse,Ndipo cipangano canga cidzalimbika pa iye.

29. Ndidzakhalitsanso mbeu yace cikhalire,Ndi mpando wacifumu wace ngati masiku a m'mwamba.

30. Ana ace akataya cilamulo canga,Osayenda m'maweruzo anga:

31. Nakaipsa malembo anga;Osasunga malamulo anga;

32. Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,Ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.

33. Koma sindidzamcotsera cifundo canga conse,Ndi cikhulupiriko canga sicidzamsowa.

34. Sindidzaipsa cipangano canga,Kapena kusintha mau oturuka m'milomo yanga.

35. Ndinalumbira kamodzi m'ciyero canga;Sindidzanamizira Davide;

36. Mbeu yace idzakhala ku nthawi yonse,Ndi mpando wacifumu wace ngati dzuwa pamaso panga.

37. Udzakhazikika ngati mwezi ku nthawi yonse,Ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.

38. Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza,Munakwiya naye wodzozedwa wanu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 89