Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 89:20-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndapeza Davide mtumiki wanga;Ndamdzoza mafuta anga oyera.

21. Amene dzanja langa lidzakhazikika naye;Inde mkono wanga udzalimbitsa.

22. Mdani sadzamuumira mtima;Ndi mwana wa cisalungamo sadzamzunza.

23. Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pace;Ndidzapandanso odana naye.

24. Koma cikhulupiriko canga ndi cifundo canga zidzakhala naye;Ndipo nyanga yace idzakwezeka m'dzina langa.

25. Ndipo ndidzaika dzanja lace panyanja,Ndi dzanja lamanja lace pamitsinje.

26. Iye adzandichula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga,Mulungu wanga, ndi thanthwe la cipulumutso canga.

27. Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba,Womveka wa mafumu a pa dziko lapansi.

28. Ndidzamsungira cifundo canga ku nthawi yonse,Ndipo cipangano canga cidzalimbika pa iye.

29. Ndidzakhalitsanso mbeu yace cikhalire,Ndi mpando wacifumu wace ngati masiku a m'mwamba.

30. Ana ace akataya cilamulo canga,Osayenda m'maweruzo anga:

31. Nakaipsa malembo anga;Osasunga malamulo anga;

32. Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,Ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.

33. Koma sindidzamcotsera cifundo canga conse,Ndi cikhulupiriko canga sicidzamsowa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 89