16. Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse;Ndipo akwezeka m'cilungamo canu.
17. Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;Ndipo potibvomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.
18. Pakuti cikopa cathu cifuma kwa Yehova;Ndi mfumuyathu kwa Woyera wa Israyeli.
19. Pamenepo munalankhula m'masompenya ndi okondedwa anu,Ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa ciphona;Ndakweza wina wosankhika mwa anthu.
20. Ndapeza Davide mtumiki wanga;Ndamdzoza mafuta anga oyera.
21. Amene dzanja langa lidzakhazikika naye;Inde mkono wanga udzalimbitsa.
22. Mdani sadzamuumira mtima;Ndi mwana wa cisalungamo sadzamzunza.
23. Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pace;Ndidzapandanso odana naye.
24. Koma cikhulupiriko canga ndi cifundo canga zidzakhala naye;Ndipo nyanga yace idzakwezeka m'dzina langa.
25. Ndipo ndidzaika dzanja lace panyanja,Ndi dzanja lamanja lace pamitsinje.