Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 89:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndidzayimbira zacifundo za Yehova nthawi yonse:Pakamwa panga ndidzadziwitsira cikhulupiriko canu ku mibadwo mibadwo.

2. Pakuti ndinati, Cifundo adzacimanga kosaleka;Mudzakhazika cikhulupiriko canu m'Mwamba mweni mweni.

3. Ndinacita cipangano ndi wosankhika wanga,Ndinalumbirira Davide mtumiki wanga:

4. Ndidzakhazika mbeu yako ku nthawi yonse,Ndipo ndidzamanga mpando wacifumu wako ku mibadwo mibadwo.

5. Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwiza zanu, Yehova;Cikhulupiriko canunso mu msonkhano wa oyera mtima.

6. Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova?Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?

7. Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri m'upo wa oyera mtima,Ndiye wocititsa mantha koposa onse akumzinga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 89