Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 87:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Maziko ace ali m'mapiri oyera.

2. Yehova akonda zipata za ZiyoniKoposa zokhalamo zonse za Yakobo.

3. Mudzi wa Mulungu, inu,Akunenerani zakukulemekezani.

4. Ndidzachula Rahabu ndi Babulo kwa iwo ondidziwa Ine;Taonani, Filistiya ndi Turo pamodzi ndi Kusi;Uyu anabadwa komweko.

5. Ndipo adzanena za Ziyoni,Uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo;Ndipo Wam'mwambamwamba ndiye aclzaukhazikitsa.

6. Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu.Uyu anabadwa komweko.

7. Ndipo oyimba ndi oomba omwe adzati,Akasupe ansa onse ali mwa inu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 87