Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 86:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mulungu, odzikuza andiukira,Ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,Ndipo sanaika Inu pamaso pao.

15. Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wacisomo,Wosapsa mtima msanga, ndi wocurukira cifundo ndi coonadi.

16. Mundibwerere ine, ndi kundicitira cifundo;Mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,Ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

17. Mundicitire cizindikilo coti cabwino;Kuti ondida acione, nacite manyazi,Popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 86