Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 86:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pakuti cifundo canu ca pa ine ncacikuru;Ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.

14. Mulungu, odzikuza andiukira,Ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,Ndipo sanaika Inu pamaso pao.

15. Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wacisomo,Wosapsa mtima msanga, ndi wocurukira cifundo ndi coonadi.

16. Mundibwerere ine, ndi kundicitira cifundo;Mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,Ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 86