Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 86:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe;Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.

2. Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.

3. Mundicitire cifundo, Ambuye;Pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.

4. Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;Pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.

5. Pakuti fnu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,Ndi wa cifundo cocurukira onse akuitana Inu.

6. Cherani khutu pemphero langa, Yehova;Nimumvere mau a kupemba kwanga,

7. Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;Popeza mudzandibvomereza.

8. Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;Ndipo palibe nchito zonga zanu.

9. Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; Nadzalemekeza dzina lanu.

10. Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakucita zodabwiza;Inu ndinu Mulungu, nokhanu.

11. Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'coonadi canu:Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

12. Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.

13. Pakuti cifundo canu ca pa ine ncacikuru;Ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 86