4. Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu;Akulemekezani cilemekezere,
5. Wodala munthu amene mphamvu yace iri mwa Inu;Mumtima mwace muli makwalala a ku Ziyoni,
6. Popyola cigwa ca kulira misozi aciyesa ca akasupe;Inde mvula: ya cizimalupsa icidzaza ndi madalitso.
7. Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,Aoneka pamaso pa Mulungu m'Ziyoni.
8. Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa:Cherani khutu, Mulungu wa Yakobo.
9. Onani, Mulungu, ndinu cikopa cathu;Ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.