Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 84:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu;Akulemekezani cilemekezere,

5. Wodala munthu amene mphamvu yace iri mwa Inu;Mumtima mwace muli makwalala a ku Ziyoni,

6. Popyola cigwa ca kulira misozi aciyesa ca akasupe;Inde mvula: ya cizimalupsa icidzaza ndi madalitso.

7. Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,Aoneka pamaso pa Mulungu m'Ziyoni.

8. Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa:Cherani khutu, Mulungu wa Yakobo.

9. Onani, Mulungu, ndinu cikopa cathu;Ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.

10. Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena,Kukhala inewapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga,Kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a coipa,

11. Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi cikopa;Yehova adzapatsa cifundo ndi ulemerero;Sadzakaniza cokoma iwo akuyenda angwiro,

12. Yehova wa makamu,Wodala munthu wakukhulupirira Inu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 84