Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 81:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Pakuti ici ndi colemba ca kwa Israyeli,Ciweruzo ca Mulungu wa Yakobo.

5. Anaciika cikhale mboni kwa Yosefe,Pakuturuka iye ku dziko la Aigupto:Komwe ndinamva cinenedwe cosadziwa ine.

6. Ndinamcotsera katundu paphewa pace:Manja ace anamasuka kucotengera.

7. Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;Ndinakubvomereza mobisalika m'bingu;Ndinakuyesa ku madzi a Meriba.

8. Tamvani, anthu anga, ndidzakucitirani mboni;Israyeli, ukadzandimvera!

9. Kwanu kusakhale mulungu wafuma kwina;Nusagwadire mulungu wacilendo.

10. Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukucotsa ku dziko la Aigupto;Yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.

11. Koma anthu anga sanamvera mau anga;Ndipo Israyeli sanandibvomera.

12. Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao,Ayende monga mwa uphungu wao wao.

13. Ha! akadandimvera anthu anga,Akadayenda m'njira zanga Israyeli!

14. Ndikadagonjetsa adani ao msanga,Ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 81