Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 81:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ha! akadandimvera anthu anga,Akadayenda m'njira zanga Israyeli!

14. Ndikadagonjetsa adani ao msanga,Ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.

15. Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga:Koma nyengo yao ikadakhala yosatha,

16. Akadawadyetsa naye tirigu wakometsetsa:Ndikadakukhutitsanso ndi uci wa m'thanthwe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 81