Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 80:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Mutiika kuti atilimbirane anzathu;Ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha,

7. Mulungu wa makamu, mutibweze;Nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

8. Mudatenga mpesa kucokera ku Aigupto:Munapitikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.

9. Mudasoseratu pookapo,Idagwiritsa mizu yace, ndipo unadzaza dziko.

10. Mthunzi wace unaphimba mapiri,Ndi nthambi zace zikunga mikungudza ya Mulungu.

11. Unatambalitsa mphanda zace mpaka kunyanja,Ndi mitsitsi yace kufikira ku Mtsinje.

12. Munapasuliranii maphambo ace,Kotero kuti onse akupita m'njira acherako?

13. Nguruwe zocokera kuthengo ziukumba,Ndi nyama za kucidikha ziudya,

14. Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu;Suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,

15. Ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaokaeNdi mphanda munadzilimbikitsira.

16. Unapserera ndi moto, unadulidwa;Aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 80