1. Mbusa wa Israyeli, cherani khutu;Inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa;Inu wokhala pa akerubi, walitsani.
2. Utsani camuna canu pamaso pa Efraimu ndi Benjamini ndi Manase,Ndipo mutidzere kutipulumutsa.
3. Mutibweze, Mulungu;Nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.
4. Yehova, Mulungu wa makamu,Mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?
5. Munawadyetsa mkate wa misozi,Ndipo munawamwetsa misozi yambiri.
6. Mutiika kuti atilimbirane anzathu;Ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha,