Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 79:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?

6. Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,Ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.

7. Pakuti anathera Yakobo,Napasula pokhalira iye.

8. Musakumbukile moritsutsa mphulupulu za makolo athu;Nsoni zokoma zanu zitikumike msanga:Pakuti tafoka kwambiri.

9. Tithandizeni Mulungu wa cipulumutso cathu,Cifukwa ca ulemerero wa dzina lanu;Ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu,Cifukwa ca dzina lanu.

10. Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao?Kubwezera cilango ca mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsaKudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu,

11. Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu;Monga mwa mphamvu yanu yaikuru lolani ana a imfa atsale;

12. Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere cotonza cao,Kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.

13. Potero ife anthu anu ndi nkhosa za pabusa panuTidzakuyamikani kosatha;Tidzafotokozera cilemekezo canu ku mibadwo mibadwo.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 79