Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 79:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mulungu, akunja alowa m'colandira canu;Anaipsa Kacisi wanu woyera;Anacititsa Yerusalemu bwinja.

2. Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhale cakudya ca mbalame za mlengalenga,Nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zirombo za m'dziko.

3. Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu;Ndipo panalibe wakuwaika.

4. Takhala cotonza ca anansi athu,Ndi coseketsa ndi colalatitsa iwo akutizinga,

5. Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?

6. Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,Ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.

7. Pakuti anathera Yakobo,Napasula pokhalira iye.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 79