Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 78:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndi kuti ciyembekezo cao cikhale kwa Mulungu,Osaiwala zocita Mulungu,Koma kusunga malamulo ace ndiko.

8. Ndi kuti asange makolo ao,Ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu;Mbadwo wosakonza mtima wao,Ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu.

9. Ana a Efraimu okhala nazo zida, oponya nao mauta,Anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo.

10. Sanasunga cipangano ca Mulungu,Nakana kuyenda m'cilamulo cace.

11. Ndipo anaiwala zocita Iye,Ndi zodabwiza zace zimene anawaonetsa.

12. Anacita codabwiza pamaso pa makolo ao,M'dziko la Aigupto ku cidikha ca Zoanu.

13. Anagawa nyanja nawapititsapo;Naimitsa madziwo ngati khoma.

14. Ndipo msana anawatsogolera ndi mtamboNdi usiku wonse ndi kuunika kwa moto.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 78