Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 78:63-72 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

63. Moto unapsereza anyamata ao;Ndi anamwali ao sanalemekezeka.

64. Ansembe ao anagwa ndi lupanga;Ndipo amasiye ao sanacita maliro.

65. Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo;Ngati ciphona cakucita nthungululu ndi vinyo.

66. Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo;Nawapereka akhale otonzeka kosatha.

67. Tero anakana hema wa Yosefe;Ndipo sanasankha pfuko la Efraimu;

68. Koma anasankha pfuko la Yuda,Phiri la Ziyoni limene analikonda.

69. Ndipo anamanga malo oyera ace ngati kaphiri,Monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha.

70. Ndipo anasankha Davide mtumiki wace,Namtenga ku makola a nkhosa:

71. Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa,Awete Yakobo, anthu ace, ndi Israyeli, colandira cace.

72. Potero anawaweta monga mwa mtima wace wangwiro;Nawatsogolera ndi luso la manja ace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 78