Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 78:44-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. Nasanduliza nyanja yao mwazi,Ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.

45. Anawatumizira pakati pao mitambo ya nchenche zakuwatha;Ndi acule akuwaononga.

46. Ndipo anapatsa mphuci dzinthu dzao,Ndi dzombe nchito yao.

47. Anapha mphesa zao ndi matalala,Ndi mikuyu yao ndi cisanu.

48. Naperekanso zoweta zao kwa matalala,Ndi ng'ombe zao kwa mphezi.

49. Anawatumizira mkwiyo wace wotentha,Kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso,Ndizo gulu la amithenga ocita zoipa.

50. Analambulira mkwiyo wace njira;Sanalekerera moyo wao usafe,Koma anapereka moyo wao kumliri;

51. Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Aigupto,Ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu:

52. Koma anaturutsa anthu ace ngati nkhosa,Nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'cipululu.

53. Ndipo anawatsogolera mokhulupirika,Kotero kuti sanaopa;Koma nyanja inamiza adani ao.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 78