40. Kawiri kawiri nanga anapikisana ndi Iye kucigwako,Nammvetsa cisoni m'cipululu.
41. Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu,Nacepsa Woyerayo wa Israyeli.
42. Sanakumbukila dzanja lace,Tsikuli anawaombola kwa msautsi.
43. Amene anaika zizindikilo zace m'Aigupto,Ndi zodabwiza zace ku cidikha ca Zoanu;
44. Nasanduliza nyanja yao mwazi,Ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.
45. Anawatumizira pakati pao mitambo ya nchenche zakuwatha;Ndi acule akuwaononga.
46. Ndipo anapatsa mphuci dzinthu dzao,Ndi dzombe nchito yao.
47. Anapha mphesa zao ndi matalala,Ndi mikuyu yao ndi cisanu.