Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 78:19-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu;Anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'cipululu?

20. Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendakoNdi mitsinje inasefuka;Kodi adzakhozanso kupatsa mkate?Kodi adzafunira anthu ace nyama?

21. Cifukwa cace Yehova anamva, nakwiya;Ndipo anayatsa moto pa Yakobo,Ndiponso mkwiyo unakwera pa Israyeli;

22. Popeza sanakhulupirira Mulungu,Osatama cipulumutso cace.

23. Koma analamulira mitambo iri m'mwamba,Natsegula m'makomo a kumwamba.

24. Ndipo anawabvumbitsira mana, adye,Nawapatsa tirigu wa kumwamba.

25. Yense anadya mkate wa omveka:Anawatumizira cakudya cofikira,

26. Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa:Natsogoza mwela ndi mphamvu yace.

27. Ndipo anawabvumbitsira nyama ngati pfumbi,Ndi mbalame zouluka ngati mcenga wa kunyanja:

28. Ndipo anazigwetsa pakati pa misasa yao,Pozungulira pokhala iwo.

29. Potero anadya nakhuta kwambiri;Ndipo anawapatsa cokhumba iwo.

30. Asanathe naco cokhumba cao,Cakudya cao ciri m'kamwa mwao,

31. Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira,Ndipo anapha mwa onenepa ao,Nagwetsa osankhika a Israyeli.

32. Cingakhale ici conse anacimwanso,Osabvomereza zodabwiza zace.

33. Potero anathera masiku ao ndi zopanda pace,Ndi zaka zao mwa mantha.

34. Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye;Nabwerera, nafunitsitsa Mulungu,

35. Ndipo anakumbukila kuti Mulungu ndiye thanthwe lao,Ndi Mulungu Wam'mwambamwamba Mombolo wao.

36. Koma anamsyasyalika pakamwa pao,Namnamiza ndi lilime lao.

37. Popeza mtima wao sunakonzekera Iye,Ndipo sanakhazikika m'cipangano cace.

38. Koma Iye pokhala ngwa cifundo,Anakhululukira coipa, osawaononga;Nabweza mkwiyo wace kawiri kawiri,Sanautsa ukali wace wonse.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 78