Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 78:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Anang'alula thanthwe m'cipululu,Ndipo anawamwetsa kocuruka monga m'madzi ozama.

16. Anaturukitsa mitsinje m'thanthwe,Inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje.

17. Koma anaonjeza kuincimwira Iye,Kupikisana ndi Wam'mwambamwamba m'cipululu.

18. Ndipo anayesa Mulungu mumtimamwaoNdi kupempha cakudya monga mwa kulakalaka kwao.

19. Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu;Anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'cipululu?

20. Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendakoNdi mitsinje inasefuka;Kodi adzakhozanso kupatsa mkate?Kodi adzafunira anthu ace nyama?

21. Cifukwa cace Yehova anamva, nakwiya;Ndipo anayatsa moto pa Yakobo,Ndiponso mkwiyo unakwera pa Israyeli;

22. Popeza sanakhulupirira Mulungu,Osatama cipulumutso cace.

23. Koma analamulira mitambo iri m'mwamba,Natsegula m'makomo a kumwamba.

24. Ndipo anawabvumbitsira mana, adye,Nawapatsa tirigu wa kumwamba.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 78