8. Cifundo cace calekeka konse konse kodi?Lonjezano lace lidatha kodi ku mibadwo yonse?
9. Kodi Mulungu waiwala kucita cifundo?Watsekereza kodi nsoni zokoma zace mumkwiyo?
10. Ndipo ndinati, Cindilaka ici;Koma ndikumbukila zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.
11. Ndidzakumbukila zimene adazicita Ambuye;Inde, ndidzakumbukila zodabwiza zanu zoyambira kale.
12. Ndipo ndidzalingalira nchito yanu yonse,Ndi kulingalirabe zimene munazicita Inu.
13. Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu;Mulungu wamkuru ndani monga Mulungu?
14. Inu ndinu Mulungu wakucita codabwiza;Munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.
15. Munaombola anthu anu ndi mkonowanu,Ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.
16. Madziwo anakuonani Mulungu;Anakuonani madziwo; anacita mantha:Zozama zomwe zinanjenjemera,