13. Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu;Mulungu wamkuru ndani monga Mulungu?
14. Inu ndinu Mulungu wakucita codabwiza;Munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.
15. Munaombola anthu anu ndi mkonowanu,Ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.
16. Madziwo anakuonani Mulungu;Anakuonani madziwo; anacita mantha:Zozama zomwe zinanjenjemera,
17. Makongwa anatsanula madzi;Thambo lidamvetsa liu lace;Mibvi yanu yomwe inaturukira.
18. Liu la bingu lanu linatengezanatengezana;Mphezi zinaunikira ponse pali anthu;Dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19. Njira yanu inali m'nyanja,Koyenda Inu nku madzi akulu,Ndipo mapazi anu sanadziwika.
20. Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa,Ndi dzanja la Mose ndi Aroni,