1. Ndidzapfuulira kwa Mulungu ndi mau anga;Kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzandicherezera khutu.
2. Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye:Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka;Mtima wanga unakanakutonthozedwa.
3. Ndikumbukila Mulungu ndipo ndibvutika;Ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.
4. Mundikhalitsa maso;Ndigwidwa mtima wosanena kanthu.